10 Iri kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?
11 Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamcotsanso m'ukali wanga.
12 Mphulupulu ya Efraimu yamangika, cimo lace lisungika.
13 Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asacedwe mobalira ana.
14 Ndidzawaombola ku, mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako iri kuti? manda, cionongeko cako ciri kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
15 Cinkana abala mwa abale ace, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kucokera kucipululu; ndi gwero lace lidzaphwa, ndi kasupe wace adzauma, adzafunkha cuma ca akatundu onse ofunika.
16 Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wace; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.