1 Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wocitidwa-cifundo.
2 Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo acotse zadama zace pankhope pace, ndi zigololo zace pakati pa maere ace;
3 ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
4 ndipo ana ace sindidzawacitira cifundo; pakuti iwo ndiwo ana acigololo.
5 Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.
6 Cifukwa cace taonani, ndidzacinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ace.
7 Ndipo adzatsata omkonda koma osawakumika, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.