5 Cifukwa cace ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga aturuka ngati kuunika.
6 Pakuti ndikondwera naco cifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.
7 Koma iwo analakwira cipangano ngati Adamu, m'mene anandicitira monyenga.
8 Gileadi ndiwo mudzi wa ocita zoipa, wa mapazi a mwazi.
9 Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi acita coipitsitsa.
10 M'nyumba ya Israyeli ndinaona cinthu coopsetsa; pamenepo pali citole ca Efraimu; Israyeli wadetsedwa.
11 Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.