1 M'mene ndiciritsa Israyeli, mphulupulu ya Efraimu ibvumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti acita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala manca kubwalo.
2 Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukila zoipa zao zonse; tsopano macitidwe ao awazinga; ali pamaso panga,
3 Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.
4 Acigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wooca mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
5 Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lace pamodzi ndi oseka.
6 Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; wooca mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi.