6 Pakuti ici comwe cafumira kwa Israyeli; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwana wa ng'ombe wa Samariya adzaphwanyika-phwanyika.
7 Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.
8 Israyeli wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati cotengera coti munthu sakondwera naco.
9 Pakuti anakwera kumka ku Asuri, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wace; Efraimu walembera omkonda ngati anchito.
10 Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kucepa cifukwa ca katundu wa mfumu ya akalonga.
11 Popeza Efraimu anacurukitsa maguwa a nsembe akucimwako, maguwa a nsembe omwewo anamcimwitsa.
12 Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za cilamulo canga, koma zinayesedwa ngati cinthu cacilendo.