13 Efraimu, monga ndaona, akunga Turo, wookedwa pokoma; koma Efraimu adzaturutsira ana ace wakuwaphera.
14 Apatseni, Yehova; mudzapatsa ciani? muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.
15 Coipa cao conse ciri m'Giligala; pakutipamenepo ndinawada, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe ao ndidzawainga kuwacotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.
16 Efraimu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.
17 Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvera Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.