1 Ndine duwa lofiira la ku Saroni,Ngakhale kakombo wa kuzigwa.
2 Ngati kakombo pakati pa mingaMomwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.
3 Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango,Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna.Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wace,Zipatso zace zinatsekemera m'kamwa mwanga.
4 Anandifikitsa ku nyumba ya vinyo,Mbendera yace yondizolimira inali cikondi.
5 Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula,Pakuti ndadwala ndi cikondi.
6 Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu,Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.