11 Pakuti, taona, cisanu catha,Mvula yapita yaleka;
12 Maluwa aoneka pansi;Nthawi yoyimba mbalame yafika,Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;
13 Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima,Mipesa niphuka,Inunkhira bwino.Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
14 Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka,Ndipenye nkhope yako, ndimve manako;Pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.
15 Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono, amene akuononga minda yamipesa;Pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.
16 Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wace:Aweta zace pakati pa akakombo,
17 Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,Bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawalaPa mapiri a mipata.