6 Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu,Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.
7 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala za kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.
8 Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.
9 Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pa khoma pathu,Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.
10 Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.
11 Pakuti, taona, cisanu catha,Mvula yapita yaleka;
12 Maluwa aoneka pansi;Nthawi yoyimba mbalame yafika,Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;