8 Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace,Cifukwa ca upandu wa usiku.
9 Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsongaNdi matabwa a ku Lebano.
10 Anapanga timilongoti tace ndi siliva,Ca pansi pace ndi golidi, mpando wace ndi nsaru yakuda,Pakati pace panayalidwa za cikondi ca ana akazi a ku Yerusalemu.
11 Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu,Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace,Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.