13 Masaya ace akunga citipula cabzyalamo ndiwo,Ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:Milomo yace ikunga akakombo, pakukhapo madzi a nipa.
14 Manja ace akunga zing'anda zagolidi zoikamo zonyezimira zoti biriwiri:Thupi lace likunga copanga ca minyanga colemberapo masafiro.
15 Miyendo yace ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,Zogwirika m'kamwa mwa golidi:Maonekedwe ace akunga Lebano, okometsetsa ngati mikungudza.
16 M'kamwa mwace muli mokoma: inde, ndiye wokondweretsa ndithu.Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa,Ana akazi inu a ku Yerusalemu.