6 Ndinamtsegulira bwenzi langalo;Koma ndinampeza, bwenzi langa atacoka.Moyo wanga unalefuka polankhula iye:Ndinamfunafuna, osampeza;Ndinamuitana, koma sanandibvomera.
7 Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,Nandikantha, nanditema;Osunga maguta nandicotsera cophimba canga.
8 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza ciani?Kuti ndadwala ndi cikondi.
9 Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Kuti utilumbirira motero?
10 Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,Womveka mwa zikwi khumi.
11 Mutu wace ukunga golidi, woyengetsa,Tsitsi lace lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.
12 Ana a maso ace akunga nkhunda pambali pa mitsinje ya madzi;Otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.