17 Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.
18 Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo, Wogwira nchito ayenera kulipira kwace.
19 Pa mkulu usalandire comnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.
20 Iwo akucimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo acite mantha.
21 Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Kristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosacita kanthu monga mwa tsankhu.
22 Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
23 Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu ucite naye vinyo pang'ono, cifukwa ca mimba yako ndi zofoka zako zobwera kawiri kawiri.