20 Iwo akucimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo acite mantha.
21 Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Kristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosacita kanthu monga mwa tsankhu.
22 Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
23 Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu ucite naye vinyo pang'ono, cifukwa ca mimba yako ndi zofoka zako zobwera kawiri kawiri.
24 Zocimwa za anthu ena ziri zooneka-kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.
25 Momwemonso pali nchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.