3 ameneyo, pokhala ali cinyezimiro ca ulemerero wace, ndi cizindikilo ceni ceni ca cikhalidwe cace, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yace, m'mene adacita ciyeretso ca zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,
4 atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.
5 Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse,Iwe ndiwe Mwana wanga,Lero ine ndakubala Iwe?ndiponso,Ine ndidzakhala kwa iye Atate,Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana?
6 Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire iye angelo onse a Mulungu.
7 Ndipo za angelo anenadi,Amene ayesa angelo ace mizimu,Ndi omtumikira iye akhale lawi lamoto;
8 Koma ponena za Mwana, ati,Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;Ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.
9 Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa;Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozaniNdi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu.