1 Cifukwa cace ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukuru wotere wa mboni, titaye colemetsa ciri conse, ndi cimoli Iimangotizinga, ndipo tithamange mwacipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womariza wa cikhulupiriro cathu,
2 Yesu, ameneyo, cifukwa ca cimwemwe coikidwaco pamaso pace, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu,
3 Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ocimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.
4 Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo cimo;
5 ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana,Mwana wanga, usayese copepuka kulanga kwa Ambuye,Kapena usakomoke podzudzulidwa ndilye;
6 Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga,Nakwapula mwana ali yense amlandira.
7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu acitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wace wosamlanga?
8 Koma ngati mukhala opanda cilango, cimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.
9 Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
10 Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.
11 Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.
12 Mwa ici limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;
13 ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti cotsimphinaco cisapatulidwe m'njira, koma ciciritsidwe.
14 Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
15 ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera cisomo ca Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;
16 kuti pangakhale wacigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wace wobadwa nao mtanda umodzi wa cakudya.
17 Pakutf mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeza malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.
18 Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsya moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,
19 ndi mau a lipenga, ndi maaenedwe a mau, manenedweamene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;
20 pakuti sanakhoza kulola colamulidwaco. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;
21 ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira.
22 Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wocuruka wa angelo,
23 ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,
24 ndi kwa Yesu Nkhoswe ya cipangano catsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula cokoma coposa mwazi wa Abeli.
25 Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana iye amene anawacenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa iye wa Kumwamba;
26 amene mau ace anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.
27 Ndipo ici, cakuti kamodzinso, cilozera kusuntha kwace kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.
28 Mwa ici polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale naco cisomo, cimene tikatumikire naco Mulungu momkondweretsa, ndi kumcitira ulemu ndi mantha.
29 Pakuti 1 Mulungu wathu ndiye mota wonyeketsa.