1 Pakuti Melikizedeke uyu, Mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,
2 amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere;
3 wopanda atate wace, wopanda amace, wopanda mawerengedwe a cibadwidwe cace, alibe ciyambi ca masiku ace kapena citsiriziro ca moyo wace, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.
4 Koma tapenyani ukulu wace wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikuru, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.
5 Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira nchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa cilamulo, ndiko kwa abaleao, angakhale adaturuka m'cuuno ca Abrahamu;
6 koma iye amene mawerengedwe a cibadwidwe cace sacokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.
7 Ndipo popanda citsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkuru.
8 Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamcitira umboni kuti ali ndi moyo.
9 Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzi limodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;
10 pakuti pajapo anali m'cuuno ca atate wace, pamene Melikizedeke anakomana naye.
11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Cilevi (pakuti momwemo anthu analandira cilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?
12 Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.
13 Pakuti iye amene izi zineneka za iye, akhala wa pfuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.
14 Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anaturuka mwa Yuda; za pfuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe.
15 Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke,
16 amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;
17 pakuti amcitira umboni,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosathaMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.
18 Pakutitu kuli kutaya kwace kwa lamulo lidadza kalelo, cifukwa ca kufoka kwace, ndi kusapindulitsa kwace,
19 (pakuti cilamulo sicinacitira kanthu kakhale kopanda cirema), ndipo kulinso kulowa naco ciyembekezo coposa, cimene tiyandikira naco kwa Mulungu.
20 Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro;
21 (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma iye ndi lumbiro mwa iye emeoe ananena kwa iye,Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).
22 Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.
23 Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;
24 koma iye cifukwa kuti akhala iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika,
25 kucokera komwekoakhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nao moyo wace cikhalire wa kuwapembedzera iwo.
26 Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa, wakukhala wopitirira miyamba;
27 amene alibe cifukwa ca kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira cifukwa ca zoipa za iwo eni, yinayi cifukwa ca zoipa za anthu; pakuti ici anacita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.
28 Pakuti cilamulo cimaika akuru a ansembe anthu, okhala naco cifoko; koma mau a lumbirolo, amene anafika citapita cilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda cirema ku nthawi zonse.