1 mthunzi wa zokoma zirinkudza, osati cifaniziro ceni ceni ca zinthuzo, sicikhozatu, ndi nsembe zomwezi caka ndi caka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.
2 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, cifukwa otumikirawo sakadakhala naco cikumbu mtima ca macimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?
3 Komatu mu izizo muli cikumbukiro ca macimo caka ndi caka.
4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndimbuzi ukacotsera macimo.
5 Mwa ici polowa m'dziko lapansi, anena,Nsembe ndi copereka simunazifuna,Koma thupi munandikonzera Ine.
6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunakondwera nazo;
7 Pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,(Pamutu pace pa buku palembedwa za Ine)Kudzacita cifuniro canu, Mulungu,
8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),
9 pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico.
10 Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.
11 Ndipotu wansembe ali yenseamaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo;
12 koma iye, m'mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire;
13 kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace.
14 Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa.
15 Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena,
16 ici ndi cipangano ndidzapangana nao,Atapira masiku ajawo, anena Ambuye:Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;
17 Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.
18 Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwaucimo.
19 Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,
20 pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa cocinga, ndico thupi lace;
21 ndipo popeza tiri naye wansembe wamkuru wosunga nyumba ya Mulungu;
22 tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
23 tigwiritse cibvomerezo cosagwedera ca ciyembekezo cathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
24 ndipo tiganizirane wina ndi mnzace kuti tifulumizane ku cikondano ndi nchito zabwino,
25 osaieka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika.
26 Pakuti tikacimwa ife eni ace, titatha kulandira cidziwitso ca coonadi, siitsalanso nsembe ya kwa macimo,
27 koma kulindira kwina koopsa kwa ciweruziro, ndi kutentha kwace kwa mota wakuononga otsutsana nao.
28 Munthu wopeputsa cilamulo ca Mose angofa opanda cifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:
29 ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa cipangano umene anayeretsedwa nao cinthu wamba, z nacitira cipongwe Mzimu wa cisomo;
30 pakuti timdziwa iye amene anati, 1 Kubwezera cilango nkwanga, loe ndidzabwezera. Ndiponso; 2 Ambuye adzaweruza anthu ace.
31 3 Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.
32 Koma tadzikumbursani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa 4 mudapirira citsutsano cacikuru ca zowawa;
33 pena pocitidwa 5 cinthu cooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ocitidwa zotere.
34 Pakuti 6 munamva cifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa cuma canu, 7 pozindikira kuti muli naco nokha cuma coposa caeikhalire.
35 Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli naco cobwezera mphotho cacikuru.
36 Pakuti cikusowani cipiriro, kuti 8 pamene mwacita cifuniro ca Mulungu, mukalandire lonjezano.
37 9 Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono,Ndipowakudzayoadzafika, wesacedwa.
38 10 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wocokera m'cikhulupiriro:Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwaiye.
39 Koma ife si ndife 11 a iwo akubwerera kulowa citayiko; koma 12 a iwo a cikhulupiriro ca ku cipulumutso ca moyo.