Ahebri 5 BL92

1 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amaikika cifukwa ca anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, cifukwa ca macimo:

2 akhale wokhoza kumva cifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi cifoko;

3 ndipo cifukwa caceco ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe cifukwa ca macimo.

4 Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wace, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.

5 Koteronso Kristu sanadzilemekeza yekha ayesedwe Mkuluwansembe, komatu iye amene analankhula kwa iye,Mwana wanga ndi Iwe, Lero Ine ndakubala Iwe;

6 Monga anenanso mwina,Iwe ndiwe wansembe wa nthawizonseMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.

7 Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,

8 angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;

9 ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera iye cifukwa ca cipulumutso cosatha;

10 wochedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

11 Za iye tirinao mau ambiri kuwanena, ndiotilaka powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.

12 Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi cifukwa ca nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za ciyambidwe ca maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati cakudya cotafuna.

13 Pakuti yense wakudya mkaka alibe cizolowezi ca mau a cilungamo; pakuti ali khanda.

14 Koma cakudya cotafuna ciri ca anthu akulu misinkhu, amene mwa kucita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa cabwino ndi coipa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13