Ahebri 3 BL92

Kristu ali wamkuru woposa Mose, Awacenjeza amkhulupirire

1 Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi. Mkuluwansembe wa cibvomerezo cathu, Yesu;

2 amene anakhala wokhulupirika kwa iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yace yonse.

3 Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.

4 Pakuti nyumba iri yonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.

5 Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yace yonse, monga mnyamata, acitire umboni izi zidzalankhulidwazi;

6 koma Kristu monga mwana, wosunga nyumba yace; ndife nyumba yace, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa ciye-I mbekezoeo, kucigwira kufikira citsiriziro.

7 Momwemo, monga anena Mzimu Woyera,Lero ngati mudzamva mau ace,

8 Musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo,Monga muja tsiku la ciyesero m'cipululu,

9 Cimene makolo anu anandiyesa naco,Ndi kundibvomereza,Naona nchito zanga zaka makumi anai.

10 Momwemo ndinakwiya nao mbadwouwu,Ndipo ndinati, Nthawi zonse amasocera mumtima;Koma sanazindikira njira zangaiwowa;

11 Monga ndinalumbira m'ukali wanga:Ngati adzalowa mpumulo wanga!

12 Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;

13 komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene paehedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi cenjerero la ucimo;

14 pakuti takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa ciyambi ca kutama kwathu kucigwira kufikira citsiriziro;

15 umo anenamo,Lero ngati mudzamva mau ace,Musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.

16 Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adaturuka m'Aigupto ndi Mose?

17 Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adacimwawo, amene matupi ao adagwa m'cipululu?

18 Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wace?

19 Si awo kodiosamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kulowa cifukwa ca kusakhulupirira.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13