1 Koma cikhulupiriro ndico cikhazikitso ca zinthu zoyembekezeka, ciyesero ca zinthu zosapenyeka.
2 Pakuti momwemo akulu anacitidwa umboru.
3 Ndi cikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zocokera mwa zoonekazo.
4 Ndi cikhulupiriro Abeli anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kami, mene anacitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nacitapo umboni Mulungu pa mitulo yace; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.
5 Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;
6 koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.
7 Ndi cikhulupiriro Nowa, pocenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pocita mantha, anamanga cingalawa ca kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yace; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa cilungamo ciri monga mwa cikhulupiriro.
8 Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kuturuka kunka ku malo amene adzalandira ngati colowa; ndipo anaturuka wosadziwa kumene akamukako.
9 Ndi cikhulupiriro anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lace, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;
10 pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wace ndi womanga wace ndiye Mulungu.
11 Ndi cikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yace, popeza anamwerengera wokhulupirika iye amene adalonjeza;
12 mwa icinso kudacokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mcenga, uli m'mbali mwa nyanja, osawerengeka.
13 Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
14 Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.
15 Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17 Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;
18 amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa:
19 poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kucokera komwe, paciphiphiritso, anamlandiranso.
20 Ndi cikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zirinkudza,
21 Ndi cikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yace.
22 Ndi cikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anachula za maturukidwe a ana a Israyeli; nalamulira za mafupa ace.
23 Ndi cikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa cilamuliro ca mfumu.
24 Ndi cikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kuchedwa mwana wace wa mwana wamkazi wa Farao;
25 nasankhula kucitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;
26 nawerenga thonzo la Kristu cuma coposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera cobwezera ca mphotho.
27 Ndi cikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika monga ngari kuona wosaonekayo.
28 Ndi cikhulupiriro 1 anacita Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
29 Ndi cikhulupiriro 2 anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aaigupto poyesanso anamizidwa.
30 Ndi cikhulupiriro 3 malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.
31 Ndi cikhulupiriro 4 Rahabi wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.
32 Ndipo ndinene cianinso? pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za 5 Gideoni, 6 Baraki, 7 Samsoni, 8 Yefita; za 9 Davide, ndi 10 Samueli ndi aneneri;
33 amene mwa cikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anacita cilungamo, analandira malonjezano, 11 anatseka pakamwa mikango,
34 12 nazima mphamvu ya moto, 13 napulumuka lupanga lakuthwa, 14 analimbikitsidwa pokhala ofok a, anakula mphamvu kunkhondo, 15 anapitikitsa magulu a nkhondo yacilendo.
35 16 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo 17 ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,
36 kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi 18 kuwatsekera m'ndende;
37 19 anaponyedwa miyala, anacekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda obvala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ocitidwa zoipa,
38 (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi 20 m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.
39 Ndipo iwo onse 21 adacitidwa umboni mwa cikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo,
40 22 popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.