16 ici ndi cipangano ndidzapangana nao,Atapira masiku ajawo, anena Ambuye:Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;
17 Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.
18 Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwaucimo.
19 Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,
20 pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa cocinga, ndico thupi lace;
21 ndipo popeza tiri naye wansembe wamkuru wosunga nyumba ya Mulungu;
22 tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;