32 Koma tadzikumbursani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa 4 mudapirira citsutsano cacikuru ca zowawa;
33 pena pocitidwa 5 cinthu cooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ocitidwa zotere.
34 Pakuti 6 munamva cifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa cuma canu, 7 pozindikira kuti muli naco nokha cuma coposa caeikhalire.
35 Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli naco cobwezera mphotho cacikuru.
36 Pakuti cikusowani cipiriro, kuti 8 pamene mwacita cifuniro ca Mulungu, mukalandire lonjezano.
37 9 Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono,Ndipowakudzayoadzafika, wesacedwa.
38 10 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wocokera m'cikhulupiriro:Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwaiye.