1 Koma cikhulupiriro ndico cikhazikitso ca zinthu zoyembekezeka, ciyesero ca zinthu zosapenyeka.
2 Pakuti momwemo akulu anacitidwa umboru.
3 Ndi cikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zocokera mwa zoonekazo.
4 Ndi cikhulupiriro Abeli anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kami, mene anacitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nacitapo umboni Mulungu pa mitulo yace; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.