10 pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wace ndi womanga wace ndiye Mulungu.
11 Ndi cikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yace, popeza anamwerengera wokhulupirika iye amene adalonjeza;
12 mwa icinso kudacokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mcenga, uli m'mbali mwa nyanja, osawerengeka.
13 Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
14 Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.
15 Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.