12 mwa icinso kudacokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mcenga, uli m'mbali mwa nyanja, osawerengeka.
13 Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
14 Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.
15 Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17 Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;
18 amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa: