16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17 Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;
18 amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa:
19 poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kucokera komwe, paciphiphiritso, anamlandiranso.
20 Ndi cikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zirinkudza,
21 Ndi cikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yace.
22 Ndi cikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anachula za maturukidwe a ana a Israyeli; nalamulira za mafupa ace.