24 Ndi cikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kuchedwa mwana wace wa mwana wamkazi wa Farao;
25 nasankhula kucitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;
26 nawerenga thonzo la Kristu cuma coposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera cobwezera ca mphotho.
27 Ndi cikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika monga ngari kuona wosaonekayo.
28 Ndi cikhulupiriro 1 anacita Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
29 Ndi cikhulupiriro 2 anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aaigupto poyesanso anamizidwa.
30 Ndi cikhulupiriro 3 malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.