14 Pakuti pano tiribe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.
15 Potero mwa iye tipereke ciperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo cipatso ca milomo yobvomereza dzina lace.
16 Koma musaiwale kucitira cokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulunguakondweranazo.
17 Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akacite ndi cimwemwe, osati mwacisoni: pakuti ici sicikupindulitsani inu.
18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri naco cikumbu mtima cokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.
19 Ndipo ndikudandaulirani koposa kucita ici, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.
20 Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,