2 Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo colakwira ciri conse ndi cosamvera calandira mphotho yobwezera yolungama,
3 tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala cipulumutso cacikuru cotero? cimene Ambuye adayamba kucilankhula, ndipo iwo adacimva anatilimbikitsira ife;
4 pocita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikilo, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundu mitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa cifuniro cace.
5 Pakuti sanagoniersera angelo dziko lirinkudza limene tinenali.
6 Koma wina anacita umboni pena, nati,Munthu nciani kuti mumkumbukila iye?Kapena mwana wa munthu kuti muceza naye?
7 Munamcepsa pang'ono ndi angelo,Mudambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu,Ndipo mudamuika iye wovang'anira nchito za manja anu;
8 Mudagonjetsa zonse pansi pa mapaziace.Pakuti muja adagonietsa zonse kwa iye, sanasiyapo kanthu kosamgoniera iye. Koma sitinayamba tsopano apa kuona zonse zimgonjera.