8 Musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo,Monga muja tsiku la ciyesero m'cipululu,
9 Cimene makolo anu anandiyesa naco,Ndi kundibvomereza,Naona nchito zanga zaka makumi anai.
10 Momwemo ndinakwiya nao mbadwouwu,Ndipo ndinati, Nthawi zonse amasocera mumtima;Koma sanazindikira njira zangaiwowa;
11 Monga ndinalumbira m'ukali wanga:Ngati adzalowa mpumulo wanga!
12 Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
13 komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene paehedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi cenjerero la ucimo;
14 pakuti takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa ciyambi ca kutama kwathu kucigwira kufikira citsiriziro;