3 ndipo cifukwa caceco ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe cifukwa ca macimo.
4 Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wace, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.
5 Koteronso Kristu sanadzilemekeza yekha ayesedwe Mkuluwansembe, komatu iye amene analankhula kwa iye,Mwana wanga ndi Iwe, Lero Ine ndakubala Iwe;
6 Monga anenanso mwina,Iwe ndiwe wansembe wa nthawizonseMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.
7 Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,
8 angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;
9 ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera iye cifukwa ca cipulumutso cosatha;