11 Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere cangu comweci colinga ku ciyembekezo cokwanira kufikira citsiriziro;
12 kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa cikhulupiriro ndi kuleza mtima.
13 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkuru woposa kumlumbira, analumbira pa iye yekha,
14 nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kucurukitsa ndidzakucurukitsa iwe.
15 Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.
16 Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'citsutsano cao ciri conse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
17 Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mocurukira kwa olowa a lonjezano kuti cifuniro cace sicisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;