17 Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mocurukira kwa olowa a lonjezano kuti cifuniro cace sicisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;
18 kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale naco coticenjeza colimba, ife amene tidathawira kucigwira ciyembekezo coikika pamaso pathu;
19 cimene tiri naco ngati nangula wa moyo, cokhazikika ndi colimbanso, ndi cakulowa m'katikati mwa cophimba;
20 m'mene Yesu mtsogoleri analowamo cifukwa ca ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.