2 a ciphunzitso ca ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a ciweruziro cosatha.
3 Ndipo ici tidzacita, akatilola Mulungu.
4 Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,
5 nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi irinkudza,
6 koma anagwa m'cisokero; popeza adzipaeikiranso okha Mwana wa Mulungu, namcititsa manyazi poyera.
7 Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso locokera kwa Mulungu:
8 koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; citsiriziro cace ndico kutenthedwa.