1 Ndipo cingakhale cipangano coyambaci cinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.
2 Pakuti cihema cidakonzeka, coyamba cija, m'menemo munali coikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika,
3 Koma m'kati mwa cophimba caciwiri, cihema conenedwa Malo Opatulikitsa;
4 okhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la cipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo munali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idapukayo, ndi magome a cipangano;
5 ndi pamwamba pace akerubi a ulemerero akucititsa mthunzi pacotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.
6 Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'cihema coyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;