5 koma musamafuna Beteli, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Beteli adzasanduka cabe.
6 Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi mayo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Beteli;
7 inu osintha ciweruzo cikhale civumulo, nimugwetsa pansi cilungamo,
8 Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova;
9 wakufikitsa cionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, cionongeko nicigwera linga,
10 Iwo adana naye wodzudzula kucipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.
11 Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wace.