3 Angakhale abisala pamwamba pa Karimeli, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.
4 Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwacitira coipa, si cokoma ai.
5 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzacita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Aigupto;
6 ndiye amene amanga zipinda zace zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lace pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lace ndiye Yehova.
7 Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israyeli? ati Yehova. Sindinakweza Israyeli ndine, kumturutsa m'dziko la Aigupto, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?
8 Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wocimwawo, ndipo ndidzauononga kuucotsa pa dziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova.
9 Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israyeli mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'licero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.