1 CAKA coyamba tsono ca Koresi mfumu ya ku Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,
2 Atero Koresi mfumu ya ku Perisiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo m'Yuda.
3 Ali yense mwa inu a anthu ace onse, Mulungu wace akhale naye, akwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m'Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli; Iye ndiye Mulungu wokhala m'Yerusalemu.
4 Ndipo ali yense wotsala pamalo pali ponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwace amthandize ndi siliva, ndi golidi, ndi zoweta, ndi cuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu.
5 Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu.
6 Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golidi, ndi cuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wace, pamodzi ndi nsembe zaufulu.
7 Koresi mfumu anaturutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adaziturutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yace;