8 zomwezi Koresi mfumu ya ku Perisiya anaziturutsa ndi dzanja la Miteridati wosunga cumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.
9 Kuwerenga kwace ndiko: mbizi zagolidi makumi atatu, mbizi zasiliva cikwi cimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;
10 zikho zagolidi makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina cikwi cimodzi.
11 Zipangizo zonse zagolidi ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kucokera ku Babulo kumka ku Yerusalemu.