Ezara 3:7-13 BL92

7 Anaperekanso ndarama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi cakudya, ndi cakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Turo, kuti atenge mikungudza ku Lebano, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Koresi mfumu ya Babulo.

8 Caka caciwiri tsono cakufika iwo ku nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi waciwiri, Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi ndi onse ocokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire nchito ya nyumba ya Yehova.

9 Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ace ndi abale ace, Kadimiyeli ndi ana ace, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira nchito m'nyumba ya Yehova, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.

10 Ndipo pomanga maziko a Kacisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe obvala zobvala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israyeli.

11 Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti cifundo cace ncosalekeza pa Israyeli. Napfuula anthu onse ndi cipfuu cacikuru, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.

12 Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akuru a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau akuru; koma ambiri anapfuulitsa mokondwera.

13 Potero anthu sanazindikira phokoso la kupfuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anapfuulitsa kwakukuru, ndi phokoso lace lidamveka kutari.