2 Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.
3 Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba cobvala canga, ndi maraya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndebvu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.
4 Nandisonkhanira ali yense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israyeli, cifukwa ca kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.
5 Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, cobvala canga ndi maraya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;
6 ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kucita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zacuruka pamtu pathu, ndi kuparamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba.
7 Ciyambire masiku a makolo athu taparamula kwakukuru mpaka lero lino; ndi cifukwa ca mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kucitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.
8 Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa cisomo, kutisiyira cipulumutso, ndi kutipatsa ciciri m'malo mwace mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu.