11 Ndipo Efraimu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lace lokoma; ndidzamsenzetsa Efraimu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya cibuluma cace.
12 Mudzibzalire m'cilungamo mukolole monga mwa cifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, nabvumbitsira inu cilungamo.
13 Mwalima coipa, mwakolola cosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakati watama njira yako ndi kucuruka kwa anthu ako amphamvu.
14 Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribeli; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ace.
15 Momwemo adzakucitirani Betele, cifukwa ca coipa canu cacikuru; mbanda kuca mfumu ya Israyeli idzalikhika konse.