4 Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.
5 Iye sadzabwerera kumka ku dziko la Aigupto, koma Asuri adzakhala mfumu yace, popeza anakana kubwera.
6 Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.
7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; cinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.
8 Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.
9 Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.
10 Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.