1 Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.
2 Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Cotsani mphulupulu zonse, nimulandire cokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati: ng'ombe.
3 Asuri sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitil dzanenanso kwa nchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza cifundo.
4 Ndidzaciritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamcokera.
5 Ndidzakhala kwa Israyeli ngati mame; adzacita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yace ngati Lebano.
6 Nthambi zace zidzatambalala, ndi kukoma kwace kudzanga kwa mtengo waazitona, ndi pfungo lace ngati Lebano.