6 Nthambi zace zidzatambalala, ndi kukoma kwace kudzanga kwa mtengo waazitona, ndi pfungo lace ngati Lebano.
7 Iwo okhala pansi pa mthunzi wace adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, cikumbukilo cace cidzanga vinyo wa Lebano.
8 Efraimu adzati, Ndiri ndi cianinso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndiri ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zocokera kwa Ine.
9 Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? waluntha, kuti adziwe izi? pakuti njira za Yehova ziri zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.