4 Acigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wooca mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
5 Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lace pamodzi ndi oseka.
6 Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; wooca mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi.
7 Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.
8 Efraimu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efraimu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa.
9 Alendo anatha mphamvu yace osacidziwaiye; imvi zomwe zampakiza osacidziwa iye,
10 Ndipo kudzikuza kwa Israyeli kumcitira umboni pamaso pace; koma sanabwerera kumka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ici conse.