1 Lipenga kukamwa kwako, Akudza ngati ciombankhanga, kulim bana ndi nyumba ya Yehova; cifukwa analakwira cipangano canga, napikisana naco cilamulo canga.
2 Adzapfuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisrayeli tikudziwani.
3 Israyeli wacitaya cokoma, mdani adzamlondola.
4 Analonga mafumu, koma sikunacokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golidi wao, kuti akalikhidwe.
5 Mwana wa ng'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
6 Pakuti ici comwe cafumira kwa Israyeli; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwana wa ng'ombe wa Samariya adzaphwanyika-phwanyika.
7 Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.