11 Popeza Efraimu anacurukitsa maguwa a nsembe akucimwako, maguwa a nsembe omwewo anamcimwitsa.
12 Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za cilamulo canga, koma zinayesedwa ngati cinthu cacilendo.
13 Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukila mphulupulu yao, nadzalanga zocimwa zao; adzabwerera kumka ku Aigupto.
14 Pakuti Israyeli waiwala Mlengi wace, namanga akacisit ndipo Yuda wacurukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yace moto, nudzatha nyumba zace zazikuru.