13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14 Ndaona nchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
15 Cokhotakhota sicingaongokenso; ndipo coperewera sicingawerengedwe.
16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi cidziwitso.
17 Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti icinso cingosautsa mtima.
18 Pakuti m'nzeru yambiri muli cisoni cambiri; ndi yemwe aenjezera cidziwitso aenjezera zowawa.